Chidziwitso cha Matenda a Kutupa Maso Komanso Mutu ku Nkhuku
Pali matenda otchedwa korayiza ("coryza") amene amaoneka ku nkhuku za kumidzi. Nthawi zina matendawa amatchedwanso chinfine cha nkhuku koma alimi ambiri sadziwa dzina lake. Amaoneka kawiri kawiri ku nkhuku za kumudzi. Akhoza kupha nkhuku zambili, makamaka nkhuku zazikulu, ndipo zazing'ono zimadwalanso koma zochepa.
Maonekedwe a Matendawa
- Zizindikilo: Kuyetsemula, kubanika, m'maso kukha misozi ndipo masowo amatupa, kutuluka mamina kapena madzi m'mphuno, m'kamwa ndi m'mphuno za nkhuku mumanunkha.
- Maonekedwe a ziwalo: M'maso ndi m'mphuno mumatuluka mafinya oyera kapena achikasu.
- Matendawa amayamba mwadzidzidzi komanso angathe kuyamba pang'ono pang'ono. Matenda amenewa amagwira m'mpuno ndi malo ena amene amathandiza kupuma. Amatupitsa malo ozungulira m'maso ndi mutu wonse. Amayambitsa kutsokomola ndi chifine.
- Nkhuku zingathe kudwala matendawa kwa sabata limodzi kapena kupitililapo. Nkhuku zikhoza kufa ndi matendawa.
Choyambitsa
- Kachirombo kamtundu wa "bacteria" kosawoneka ndi maso, kamene kamapezeka kwambiri muno m'Malawi.
- Chiyambi cha matendawa: Nkhuku zimapatsirana kuchokera ku madzi kapena mpweya umene zimapumarana, osaiwaranso m'chakudya.
Kuchiza
- Mankhwala a mtundu wa sulfonamides (sulfa drugs); kapena trimethoprim ndi sulfonamides; kapena ma antibiyotiki ena. Mankhwalawa amapezeka ku veterinary shops.
Kupewa
- Kuli katemera woteteza matendawa koma alimi ambili samagwritsa ntchito katemera ameneyu.
- Ndikovuta kuteteza matendawa ku nkhuku zoyendayenda chifukwa zimakumana ndi nkhuku zochokera ku malo ena. Ndikotheka kuteteza matendawa ku nkhuku zodyera m'khola poteteza nkhuku zina zodwala kubwera pafupi.
- Nkhuku zosiyana misinkhu zisakhalire pamodzi, ndipo nkhuku zokalamba zichotsedwe kapena zigulitsidwe kupewa kupatsa matenda kunkhuku zazing'ono.